ACHINYAMATA A MPINGO WA MTUNTHAMA AGAWA MABUKU 100
Achinyamata a mpingo wa Mtunthama pa 17 August 2024 anali ndi Chilinganizo Chogawa mabuku (Street Evangelism).
Chilinganizochi chinatsogodzedwa ndi atsogoleri a pa mpingowu.
Master Guide Tinyade Massi ndi Master Guide Hamphery Namakhusa analimbikitsa achinyamata onse kuti akuyenera kunyamuka kupita kukafalitsa uthenga wa Mulungu ( I will go).
Ulendo ogawa mabuku unayambila pa Puma filing Station , St Andrews Trading centre ,mtunthama trading centre ,komboni ya French kukamalizila pa msika.
Achinyamatawa atha kukwanitsa kugawa mabuku 100 , ( Chiyembekezo Chotsiriza ,Signs of Hope komanso ma pepala a VOP kwa abale ndi alongo onse omwe anakumana nawo .
Mu ulendo onsewu, mkulu wa mpingo Charles Chikuni ndi omwe adalalikira mmadera onse.
Lucas Henry
CMC Media
Comments