top of page
Pastor Petro Sukali.jpeg

KUVALA ZILIMBE. Kumela Khungu

La Njobvu

Tebulo la a Pulezidenti

Petro Lameck Sukali - President, Central Malawi Conference

Moni kwa nonse, konse komwe muli. Ndisanalankhule zambiri, ndafuna ndikulandireni ku  tsamba ili la Pulezidenti wa Central Malawi Conference (CMC).

 

Zaka zisanu zogwira ntchito, zomwe uphungu waukulu mu CMC unakhazikitsa mu chaka cha 2014, zinatha mu September 2019. Utsogoleri watsopano wapatsidwa kwa ine ndi amzanga kuyambira chaka chino cha 2019 mpaka September 2022. Sindikuchitenga ichi kukhala chophweka chifukwa ndikudziwa kuti tili ndi zobetchera kutsogolo kwathu. Chinthu chimodzi chomwe chimanditonthoza ndi kundilimbikitsa ndi chakuti; Mulungu sadzasankha munthu pa udindo osamupatsa mphamvu ndi nzeru zogwirira ntchito pa udindowo.

Ndiyamikire a Pulezidenti omwe angopuma kumene, Pastor John Phiri ndi amzawo, pa ntchito yotamandika yomwe agwira ku CMC. Anali ndi ziyang’aniro ndi masomphenya ambiri oyendetsera mpingowu. Zina zinachitika, ndipo zina zikanali kukonzedwabe. Ntchito yoyamba ikhala kupitiriza pomwe amzathuwa anasiyira ndikumalizitsa ntchito zomwe zinali zisanathe. Powonjezera, tikhazikika kwambiri pa ntchito yathu yayikulu yofikira anthu mumpingo komanso kunja ndi uthenga wabwino kuti ambiri amudziwe Mulungu koposa kale. Izi zitheka polinganiza maphunziro a wogwira ntchito ku CMC komanso mmipingo. Kuti tikhale asodzi abwino a anthu, ndikofunika tiwonetsetse kuti zipangizo zoyenera zogwirira ntchito zaperekedwa kwa anthu ndipo pali chisamaliro chabwino kwa ogwira ntchito anthu.

Monga ndanena kale, ulendowu siwophweka. Nditha kutchula mavuto ambiri omwe tingakumane nawo kutsogoloku, koma tsamba ili ndilofotokoza mayankho osati mavuto podziwa kuti zomwe tingakumane nazo lero kapena mawa sizachilendo, ena anakumana nazo kale mmbuyomu. Mlongo Ellen White, mu masomphenya ake a “Njira Yopapatiza” akutiuza kuti atsogoleri omwe anayambitsa mpingowu anakumananso ndi zobetchera ndipo anapambana chifukwa cha chikhulupiriro chawo mwa Mulungu. Mwachidule, ndikutha kuwona iwo atavala zilimbe monga imachitira njobvu. Khungu la njobvu ndilonenepa ma centimetre pakati pa 2 ndi 3 ndipo ndilokhuthala. Njobvu ikamayenda mutchire imalumidwa ndi tizilombo komanso njoka za ululu. Koma chifukwa cha chakukhuthala ndi kulimba kwa thupi lake, siyidandaula, imangopitiriza ulendo wake.

 

Ife tikufunika kukhala ndi thupi ngati ili la uzimu kuti tifikire ziyang’aniro zathu kutsogoloku. Chaka cha 2020 chikuyamba. Tikuyenera tiyambe limodzi ndi Ambuye wathu yemwe ali mfungulo wokhawo wa chipambano chathu. Nthano ya chitsamba choyaka mu buku la Eksodo ndime 3 ikuyenera kutiphunzitsa za ukulu ndi mphamvu za Mulungu. Ambiri amaganiza kuti chozizwa chinali kuyaka kwa moto. Koma khulupirirani kuti sichomwecho. Chomwe chinamudabwitsa Mose chinali choti monga momwe zikhalira, moto omwe ndiwamphamvu umayenera kunyeketsa tsamba lomwe ndilofowoka. Kusanyeka kwa tsamba ndicho chinali chozizwa. Pamapeto Mose anazindikira kuti izi zinatheka chifukwa cha Mulungu yemwe anadzitchula kuti INE NDINE. Okondedwa, tiyeni tivomereze ndikulolera kupezeka kwa Mulungu mmoyo wathu komanso mu kena kalikonse kuti tipambane munyengo zabwino komanso zovuta.

Pempho langa kwa nonse ndi lakuti, tiyeni tigwirane manja kuti mpingo wathu upambane mu CMC. Monga atsogoleri, timagwira ntchito modalirana. Yesu anapambana kale mmalo mwathu pa mtanda paja. Chotsalira kwa ife ndikuti ndithamange pa liwiro la V1 mu ntchitoyi. Kodi Liwiro la V1 ndiye liti? Mu Buku lawo Dr G Mweemba (Start Happening 2019.8) akufotokoza momwe ndege imawulukira. Akuti owulutsa ndege amayamba wachonga mndandanda wa zinthu zofunikira kuti zichitike ndege isanawuluke, akamaliza, amalengeza kwa ogwira ntchito mu ndege kuti akonzeke chifukwa ndege ikunyamuka tsopano. Panthawiyi onse ogwira ntchito mu ndege, amapita kukakhala mmipando yawo. Akatero owulutsa ndege apayima pa nsewu owulutsira ndege kudikira chilolezo.

 

Akapatsidwa chilolezo amayikonzetsera ndege kuti inyamuke, ndipo Ndege imamveka phokoso ngati ili mmalele koma isananyamuke.  Akatero amakankha chida chowulutsira ndege ndipo ndege amawonjezera liwiro, ndikuthamanga liwiro lododometsa. Zikatero, makina amatumiza Uthenga woti V1. Pakatha mawu oti V1 pamabwera mau ena oti Rotate ndipo ndege imanyamuka kupita mlengalenga.  Chotero, V1 ndi liwiro lomwe ndege imayenera ithamange kuti iwuluke. Ndipo ikuyeneradi kuwuluka. Pa V1 ndipowulukira basi, ndipo owulutsa sangasinthenso maganizo kuti ndege ibwerere; saloledwa kutero. Ngati ukufuna kusintha maganizo kuti ndege isawuluke, uchite izi usanafike pa liwiro la V1. Pilot amachotsa mkono wake pa chida chowulutsira ngege chifukwa amawopa kuti ayesedwa kuyibweza ndegeyo itafika kale pa liwiro la V1.

 

Pa liwiro la V1 ndikowopsa kusintha maganizo kuti ndege ibwerere ; kuli bwino kungopitiriza kuwuluka. Pa liwiro limeneli anthu omwe akwera ndegeyi amakhala otetezeka kwambiri ndege ikawuluka, kuyisana ndikuti ikhalebe ikuyenda pansi. Kuwopsa kobweza ndege ili pa liwiro la V1, ndikwakuti, ndege ikafika pa liwiro limeneli, nsewu womwe imayendamo  umakhalanso kuti uli kumapeto ndiponso ndegeyo siyingathe kuyima nsewuwo usanathe.  Chotsatra chake imakhala ngozi yowopsa. Ngakhale patapezeka vuto pa ndegeyo, ngati ili mu liwiro la V1 ikuyenerabe inyamuke, ndikukabwereranso pansi kuchoka mmalele. 

 

Pa liwiro la V1, ndege imakhala kuti yakonzeka kunyamuka, ndipo kuwuluka chimakhala chikakamizo. Chotero, tiyeni tiyambenso moyo wathu pa V1 pomwe titatha kuthandizidwa ndi Yesu Khristu palinenso china chingatiyimitse.

Kumbukirani 

 

Tiyeni tikhale ndi khungu lokhuthala ngati la njobvu, ndipo tithamange pa liwiro la V1 pomwe tinyamukire kupita mmwamba. Mulungu akudalitseni nonse

 

Petro Lameck Sukali, Pulezidenti wa CMC.

bottom of page