Pastor John A.G. Phiri

John A.G Phiri

CMC President

A Unique People with a Unique Purpose:

A Reminder and Call to Seventh-day Adventists in Central Malawi Conference

Anthu Apadera a Cholinga Chapadera:

Chikumbutso ndi Mwitano kwa a Seventh-day Adventist mu Sentro Malawi Konfalesi

  • Facebook Social Icon

Follow the President

Okhulupirira anzanga ndi abwenzi, Ine ndine okondwa kukulemberani uthenga uwu monga njira yokukumbutsirani cholinga chathu chimene ife tiriko kunja kuno monga a Seventh-day Adventist ndikugawana nau masomphenya athu ndi ndondomeko za momwe tigwirire ntchito monga Konfalesi pa zaka za 2016-2021

 

Ife ndife ayani?

Monga a Seventh-day Adventist timadzitenga tokha monga mdipiti waulosi kapena gulu la anthu amene adayamba monga chotsatira cha ulosi amene cholinga chathu ndi kukonzetsera dziko lapansi zakubweranso posachedwapa kwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu. Ifeyo timadziona tokha monga chiphiphiritso kapena woyimirira mmalo mwa angelo atatu aja a m’buku la Chibvumbulutso 14 amene akutengera uthenga ochenjeza ku dziko lapansi limene liri mmavuto.

 

Mwa njira ina, timakhulupirira kuti Mulungu watiyitana ife ncholinga ndipo watilamulira kuti tilalikire uthenga wa angelo atatu ndi kulengeza za chikhulupiriro cha Yesu (Mat. 28:18-21; Chibv. 14:12).

 

Kuitanidwa ku Kalalikira Uthenga Wabwino

Zimenezi zikulongosola bwino udindo wathu monga mpingo. Tayitanidwa kuti tikalalikire mau kaya “munyengo yake kapena osakhala munyengo” (2 Tim. 4:2, ESV); “kaya nzokondweretsa kaya ayi” (NET). Ndipo monga Mtumwi Paulo akunenera, “tsoka kwa [ife], ngati [siti] lalikira Uthenga wabwino ” (1 Akor. 9:16, KJV).  Mulungu akutiyembekezera ife kukwaniritsa Utumiki wa Ukulu wofalitsa Uthenga wabwino ku dziko lonse la pansi kaya tichita modzipereka tokha kapena monga ntchito imene tikuyembekezeredwa kukuitanira kwake. Umenewo ndi udindo wathu kwa Mulungu komanso kwa anthu anzathu (1 Akor 9:17d, HCSB). Nchabwino kwambiri koma titachita mosangalalira ndi modzipereka chifukwa monga mtumwi Paulo akunenera, “pakuti ngati ndichita ichi chibvomerere, mphotho ndiri nayo; koma ngati si chibvomerere, anandikhulupirira m’udindo” (1 Akor 9:17).

 

Kuitanidwa kukachirikizira Uthenga wa Bwino

Muyitaniro okalalikira Uthenga wa bwino ndi muitanironso okachirikizira kapena kuti kuthandizira mbali iriyonse ya Uthengawo. Mu Aroma 10:14-15, Paulo mobetchera akubweretsa funso lotsatirali: “Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa?”(Aroma 10:14-15, KJV). Kumafunso a Pulowa Ine ndikufuna ndionjezereko kuti “adzatumizidwa bwanji ngati palibe ndalama ndi zinthu zina zofunikira?”

 

Yankho lodziwikiratu nlakuti: nzosatheka kutumiza alalikira pamene tiribe zofunikira, makamaka makobiri. Sitingachite chitukuko cha zomanga manga zimene tikufuna pofuna kupititsira patsogolo ntchito yofalitsa uthenga wabwino ngati tiribe ndalama.

 

Fundo ndiyakuti, tifuna makobiri ngati titi tigwedeze dziko lathu potumiza ogwira ntchito a Uthenga wabwino apo bi nchimodzimodzi kungoyiwalako zoti Ambuye Yesu abweranso posachedwapa. Kumbukirani kuti m’Mateyu 24:14 Yesu adamangirira kubweranso kwake kwa chiwiri padziko lapansi kukumalizika kwake kwa kufalitsa Uthenga wabwion pa dziko lonse la pansiri. M’mau ena, ngati akuphunzira Ake, inuyo ndi ine,sitifalitsa Uthenga wabwino umenewu Yesu sabwera msanga. Koma ife siife okonzeka kumuona Yesu akuchedwa. Kapena titero kuti tikufuna zimenezo?

 

Pachifukwa chimenechi, tifuna thandizo la chuma kuti tikwaniritsire cholinga chathu ndi kuyendetsera mapologalamu osiyanasiyana amene talinganiza mundondomeko yathu yogwirira ntchito. Ife ndife adindo ndipo Mulungu akutiyembekezera kuti tigwira ntchito yake ndi kuchita moyenerera.

 

Mungatenge nawo Mbali Bwanji?

Funso lanu lodziwikiratu likhoza kukhala lakuti, nanga ndingathandize bwanji? Ndingatenge nawo mbali bwanji muntchito yapamwamba ngati imeneyi m’dera lathu lino kuti tifulumizitse kubwera kwa Ambuye Yesu?

Pali njira zambiri zimene inuyo mungatengere nawo mbali kukwaniritsa cholinga cha Mulungu mnthawi ino. Tiri ndi ziringanizo zimene tayambitsa ndi ntchito zosiyanasiyana zimene mungakonde kulowapo kukatenga mbali molingana ndi chidzi komanso kutha kwanu. Nawa ena mwa maganizo amene angakuthandizeni:

 

Go 150

Mwa chitsanzo, tiri ndi chiringanizo chotchedwa “Pitani 150” kapena “Go 150” chimene ndichiringanizo chimene cholinga chake nkufalitsa uthenga m’maboma asanu ndi limodzi a mchigawo chathu chino kumene uthenga wathu sudafalikire. Mchiringanizo chimenechi chiyang’aniro chathu nchakuti tikufuna kuchita misonkhano ija timayi ya efoti yosachepera pa 150 chaka chirichonse kwa zaka zinai zikubwerazi, ma efoti 25 m’boma lirilonse la maboma asanu ndi limodzi aja. Chiyang’aniro chachikulu chathu nchopangitsa ma efoti osachepera 100 m’maboma amenewa.

Tikuphunzitsa alaliki amene azitumidwa kumalo osiyanasiyana amene tawatumba kuti ngosafikiridwa kale kuti akalalikire kumeneko. Tikufuna thandizo la ndalama kuti izi zitheke. Mukhoza kutenga nawo mbali mu chilinganizo ichi popereka ndalama kuchilinganizochi kapena inuinu eni kupita kudera limene mungakonde m’madera amenewa kukachita efoti nokha.

 

Ngati simukufuna kuitumiza ndalama yanu kwa ife, mukhoza kungothandizira efoti kumalo alionse m’maboma amenewa. Pakali pano (mu 2016) tikuyerekeza kuti ndalama zosachepera MK200, 000.00 kapena US$350.00 zitha kukwanira kupangitsira efoti m’madera amene tawasankhawo. Mukafuna kudziwa zambiri mutha kutifunsa podzera ku: info@cmcadventist.org kapenanso mutha kuyankhulana ndi dipatimenti yathu yowona za mautumiki ofalitsa uthenga wabwino (Personal Ministries) kapenanso mukhoza kutipeza ku maofesi athu ku Area 14..

 

Zitukuko za padera za Zomangamanga

Njira ina imene mungakonde kuitsata pofuna kutenga nawo mbali mchigawo chathu chino ndiye yosankha kuchokera pa mndandanda wa zintchito zimene tazichamika kuti tizichite mnzaka zimenezi ndipo mukhoza kupereka thandizo lanu lamtundu ulionse kumeneko kaya ndi kutithandizira maganizo, njira iri yonse! Mwinanso mutha kungosankha kambali kena ka ntchito iriyonseyo imene inuyo mungakwanitse mogwirizana ndi kupeza kwanu.

 

Konfalesi yathu ikadali yakhanda mchitukuko. Tikusowa zipangizo ndi nyumba zotithandizira kuti tigwire ntchito yathu modzaza. Mwa chitsanzo, tiri ndi nyumba zochepa za abusa athu. Abusa athu ambiri amakhala mnyumba za renti zimene mapeto ake zikutitengera ndalama zambiri zimene tikadakhoza kugwiritsira ntchito kukafikira malo osafikiridwa komanso kupangira zitukuko zina. Chobetchera chathu chachikulu ndi kusowa kwa ndalama.

 

“Kachipinda ka kang’ono” (Small Room Project)

Pofuna kuthetsa vuto limeneri lakuchepa kwa nyumba za abusa tayambitsa chilinganizo chimene tikuchiti “Kachipinda kakang’ono” kapena kuti “Small Room Project.”  Ichi nchilinganizo chimene chikuchokera paganizo la pa 2 Mafumu 4:8-17 pamene mai wina wa ku Sunemu powona Elisa ndi utumiki wabwino umene amachita koma okhala ndi chosowa cha malo ogona akamagwira ntchito yake adanena kuti “Timmangire kacipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi coikapo nyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m’mwemo.” Cholinga cha chilinganizo chimenechi nkumanga nyumba zogonamo abusa athu komans a ntchito ena onse amene amathandizira ntchito yathu yofalitsa uthenga wabwino..

 

Pachilinganizo chimenechi cha “Kachipinda kakang’ono” mutha kusankha kaya kutipatsa ndalama zoti zikamangire nyumba ya abusa kapena inuinu mutha kungotimangira nyumbayo nkutipatsa kudera lirilonse limene tikadalibeko nyumba ya abusa mchigawo chathuchi. Tidzathokoza.

 

Gulobo Mishoni Payoniyara

Potsirizira, tirinso ndi chilinganizo cha ma Golobo Payaniya. Ma Gulobo Mishoni Payoniya ndi anthu, ziwalo za mpingo wathu zodzipereka amene timawatumiza titatha kuwasula kumadera kumene kulibe chi Andventist kukakhalako kwa nthawi yosachepera chaka chimodzi kapena ziwiri ndi chiyang’aniro chakuti akatsegule mpingo mderalo. Amphwereka (kapena kuti anthu odzipereka, volunteers mchingerezi) amenewa timawapatsa kandalama pang’ono kakuti kaziwathandiza kupeza chakudya ndi sopo panthawi imene akugwira ntchito imeneyi mdera limene tawatumizalo. Kuti mudziwe zambiri za malipiro awo pakali pano mutakhala ndi chidwi chofuna kuthandizapo mukhoza kutilankhula potilembera kudzera apa  kapenanso mutha kubwera ku likulu kwathu.

 

Pakali pano tinali ndi magulobo mishoni payoniya 20 amene anali mmdera osiyanasiyana koma nthawi yawo yatha. Kontirakiti yawo inatha ndipo chifukwa chosowa makobiri sitinakwanitse kutumiza ena. Koma chiyang’aniro chathu nchakuti titumize anthu okwana zana limodzi(100) kuti tifulumizitse ntchito yofikira madera osafikiridwawa. Chobetchera chathu ndi makobiri. Tiribe makobiri okwana pakali pano. Mungakonde kutithandiza potenga gulobo mission payoniya mmodzi kapena angapo amene inu mungathe kuti muzititumizira makobiri omulipirira kuti akachite ntchito imeneyi mdera lirilonse limene ife tingamtumizeko kwa chaka chimodzi kapena kwa nthawi yayitali imene inuyo mungakwanitse. Ndikukhulupirira kuti kufalitsa Uthenga Wabwino chikadali cholinga cha Mulungu kwa m’badwo wathu ndi Mpingo wathu.

 

Kuitanidwa ncholinga

Kulikonse kumene inu muli, chirichonse chimene inu muli, mungathe kuchita kenakake kamene kangathandizire kupititsa patsogolo cholinga cha Mulungu.  Kumbukirani, Mulungu akufuna kukugwiritsirani ntchito ndipo akufuna akhale mnzanu ogwirizana Naye pamene akufuna kukwaniritsa cholinga chake padziko lapansiri. Muli ololera kuti mukhale mbali ya gulu limene likufunafuna kukwaniritsa cholinga cha Mulungu padziko lapansiri?

Muli pamene mulipo chifukwa Mulungu ali ndi cholinga chapadera ndi inu. Akukufunani. Akufuna kuti mupite ndikukamchitira Iyeyo monga momwe muja adafuniranso Mfumukazi Estere munthawi yake kuti amuchitire mmalo Mwake. Mutero?

 

Monga momwe muja Mulungu kudzera mwa Moredekayi adamukumbutsa nkumuchenjeza Estere nati, “Usamayesa mumtima mwako kuti iwe ndi apabanja lako mudzapulumuka mnyumba ya mfumu koposa a Yuda ena onse. Pakuti ukakhala chete panthawi ino, ndiye kuti chithandizo ndi chipulumutso kwa a Yuda chibwera kuchokera kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate ako mudzaonongeka: ndipo adziwa n’ndani kuti kapena mwina iwe udabwerera ku ufumuwu chifukwa cha nyengo ngati imeneyi? (Estere 4:13-14, kumasulira kwa ndekha), Mulungu lero akufunsanso inu chimodzimodzi kuti, “Adziwa n’ndani kuti mudabwerera ku ufumuwu chifukwa cha nyengo yonga imeneyi…?”

 

Mmawu ena, Mulungu wakupangani inu chimene muliricho ndi cholinga. Akufuna akugwiritsireni ntchito mkukweza ntchito Yake.

 

Mwayi Okatumikira

Nawu pano mwayi wanu oti mungathe kukaonetsera chikondi chanu pa Mulungu ndi ntchito Yake komanso Mpingo Wake. Mungathe kutenga nawo mbali. Ichi nchifukwa chake ndikukuyitanirani kuti Bwerani kuno, ndipo thamangani ncholinga.

 

Zonsezi zikuperekedwa monga mbali imodzi yokwaniritsira chilinganizi cha Chiwalo chirichonse Kutenga Mbali (Total Member Involvement) chimene nchilinganizo chimene udayambitsa mpingo wathu pa msonkhano wake wa ukulu wa Genero Konfalensi Seshoni wa 2015 ku San Antonio ku Amerika. Mungathe kupeza mndanda okwana wa zilinganizo zosiyanasiyana ndi ntchito zimene pakali pani Konfalesi yathu ikulimbikitsa ndi kuchita apa . 

 

Kuitanidwa kukathamanga pa Cholinga cha Mulungu

Mulungu akutiyitana tonsefe kuti tikatsatire ndi kukwaniritsa cholinga chake ndipo palibenso china chirichonse chimene chimmapanga munthu wina aliyense kukhala wapadera pamaso pa Mulungu kuposera kuthamanga pacholinga cha Mulunguyo. Kuthamanga pa cholinga cha Mulungu ndi chinthu chokhacho chotetezeka chimene tikhoza kuchita.Chimatitsimikizira ife za kukhala nafe Kwake ndi kupezeka kwake kosalephera nthawi zonse. Yesu adati, “Atate anga sadandisiye ndekhandekha; chifukwa nthawi zonse ndimachita zinthu izo zimene zimamukondweretsa iye.” (Yohane 9:29, kumasulira kwanga).

 

Ndikukhulupirira kuti kufalitsa Uthenga Wabwino chikadali cholinga cha Mulungu kwa m’badwo wathu ndi Mpingo wathu ndipo tonsefe tiyenera kujijirika potenga nawo mbali munjira ina ndi inzake. Monga utsogoleri wa Konfalesi, ife tatsimikizika kuthamanga pa cholinga cha Mulungu ndipo tatsimikizika kukaona kuti Uthenga Wabwinowu ufalikire mofulumira mdera lathuli ngakhalenso kudutsa pamenepo.

 

Kuitanidwa Kukakula kuchoka pa Ophunzira kukakhala Atumwi

Kuposera pongoyitanidwa kudzakhala akuphunzira a Yesu, Mulungu akufuna ife tikhale atumwi Ake kudziko lapansi limene likufua mu uchimo. Mwitano wa Ulamuliro waukulu (The Great Commission call) ndi mwitano omveka bwino ndi owonekeratu wa Ambuye wathu wosuntha otsatira Ake kuchoka pa kuphunzira kupita ku kutumikira, μαθητής (mathētēs) kupita kukhala ἀπόστολος (apostolos) umene Ambuye wathu Yesu akadapitiriza kupanga.

Kwa nthawi yayitali mpingo wayika chigogomezo chake kwambiri pa za uphunzira (discipleship) koposa pa za utumwi (apostleship) ndipo palibe cholakwikwa chirichonse pakutero. Komabe, chinthu china chamtengo wake chatayidwa kapena kusukulutsidwa pakutero pamene a Khristu ambiri angokhala okwanitsidwa nkukhala kapena kumatchedwa kuti ophunzira a Yesu bola ali ndi chidziwitso chonse cholondola chimene ma seminare awo ndi masukulu ophunzirirako za umulungu ali nacho. Siwokonzeka ndi kulolera kuyika miyoyo yawo pachiswe monga amachitira atumwi chifukwa cha Ambuye amene amati amamukonda pomapita kunja kukagawana ndi ena ndi kuchitira umboni za choonadi ku dziko limene likufali. Chimenechi chachedwetsa kukula kwa Chikhristu makamaka chi Adventist mmalo ambiri a dziko lapansi, kuphatikizapo mdera lathu lino.

 

Koma mukamawerenga Chipangano cha Tsopano, mungagwirizane nane kuti akuphunzira khumi ndi awiri aja a Yesu sadakhale akuphunzira kwa muyaya. Adaasuntha kuchoka pokhala akuphunzira kukhala Atumwi. Pali kusuntha kuchokera pokhala akuphunzira wamba kupita pokhala atumwi. Buku la Machitidwe a Atumwi limaulula zimenezi moonekera kwambiri.

 

Ophunzira “zimalozera kwa “mphunzi” aliyense, “mwana wa sukulu,” “ophunzirira ntchito” kapena “otsatira” posiyanitsa ndi “mphunzitsi””

 

Mtumwi, mbali inayi, ndi munthu, kaya ophunzira kapena wina aliyense amene watumidwa ndi wina kukachita ntchito ina yake.

 

Koma liu lakuti ἀπόστολος (apostolos), “ngakhale limatenga ganizo la wamba la wamithenga, “ liri ndi tanthauzo lolimbirapo kuposa wamithenga , kutanthauza munthu amene wapatsidwa ntchito yokachita kunja, ndi mphamvu za ulamuliro za omtumayo. Mchipangano cha kale cholembedwa mchiGiriki liu limeneri limapezeka kamodzi mu 3 Mafumu 14:6...Kumasulira kwake m Chingerezi nkwakuti, Ine ndatumidwa kwa inu…” (DR) kapena "Ndalamuliridwa kukupatsani inu…" (NAB)”

 

Ndikuganiza kuti atumwi koposa ophunzira ndi chimene Yesu akutifuna tonsefe kuti tikhale. Uphunzira simapeto mwaiwo okha. Imeneyo ndi njira chabe yolinga kumapeto. Mulungu akufuna inu ndi ine kuti tituluke kunja ndikukagawa nkhani yabwino ya chipulumutso. Watipatsa ulamuliro wake ndikutituma kuti tikalikonzetsere dziko lapansili za kubweranso kwake kwa chiwiri.

 

Chotero ndikukubetcherani lero, kuti bwerani kuno, dzathamangeni ncholinga; dzakhale nafeni limodzi; thamangani pa cholinga cha Mulungu ndi kuchitira umboni chifuniro chake chikukwanitsidwa mwa inu ndipo onani Ufumu wake ukufika. Yimirirani Yesu ndipo tengani gawo lotakataka mkufalitsa Ufumu wake. Mudzachita ichi? Zikomo!